Levitiko 14:52-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. nayeretsenyumbandi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.

53. Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aicitire coitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.

54. Ici ndi cilamulo ca nthenda iri yonse yakhate, ndi yamfundu;

55. ndi ya khate la cobvala, ndi la nyumba;

56. ndi yacotupa, ndi yankhanambo, ndi yacikanga;

57. kulangiza tsiku loti cikhala codetsa, ndi tsiku loti cikhala coyera; ici ndi cilamulo ca khate.

Levitiko 14