Levitiko 13:48-55 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

48. ngakhale iri pamuyaro, kapena pamtsendero, cathonje, kapena caubweya, ngakhale iri pa cikopa, kapena pa cinthu ciri conse copanga ndi cikopa;

49. ngati nthenda iri yobiriwira, kapena yofiira pacobvala, kapena pacikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;

50. ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse ciija ca nthenda masiku asanu ndi awiri;

51. naone nthenda tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati nthenda yakula pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pacikopa, ziri zonse zanchito zopangika ndi cikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndico codetsedwa.

52. Ndipo atenthe cobvalaco ngakhale muyaro wace, ngakhale mtsendero wace, caubweya kapena cathonje, kapena ciri conse cacikopa ciri ndi khate, ndilo khate lofetsa; acitenrhe ndi mote.

53. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pacobvala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa;

54. pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke cija pali khate, nacibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55. ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ace, yosakulanso nthenda, ndico codetsedwa; ucitenthe ndi moto; ndilo pfunka, kungakhale kuyera kwace kuli patsogolo kapena kumbuyo.

Levitiko 13