45. Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndikhale Mulungu wanu; cifukwa cace mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.
46. Ici ndi cilamulo ca nyama, ndi ca mbalame, ndi ca zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi ca zamoyo zonse zakukwawa pansi;
47. kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.