Levitiko 11:23-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.

24. Ndipo izi zikudetsani: ali yense akhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;

25. ndipo ali yense akanyamulako nyama ya mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

26. Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.

27. Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28. Ndipo iye amene akanyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.

Levitiko 11