10. Koma ziti zonse ziribe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse ziri m'madzi, muziziyesa zonyansa;
11. inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.
12. Ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa.
13. Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi;
14. ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wace;
15. kungubwi mwa mtundu wace;
16. ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi mwa mtundu wace;
17. ndi nkhutunkhutu ndi nswankhono ndi mancici;