Hoseya 12:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Yakobo anathawira ku thengo la Aramu, ndi Israyeli anagwira nchito cifukwa ca mkazi, ndi cifukwa ca mkazi anaweta nkhosa.

13. Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israyeli kucokera m'Aigupto, ndi mwa mneneri anasungika.

14. Efraimu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wace, ndi Ambuye wace adzambwezera comtonza cace.

Hoseya 12