5. monga momwe ndinapangana nanu muja munaturuka m'Aigupto, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu.
6. Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;
7. ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.
8. Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu.
9. Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.
10. Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wacisanu ndi cinai, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,