1. Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku la makumi awiri ndi cimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,
2. Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti,
3. Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wace woyamba? ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati cabe?
4. Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kucita; pakui. Ine ndiri pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;