Genesis 7:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo analowa Nowa ndi ana ace ndi mkazi wace ndi akazi a ana ace m'cingalawamo, cifukwa ca madzi a cigumula.

8. Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,

9. zinalowa ziwiri ziwiri kwa Nowa m'cingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.

10. Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a cigumula anali pa dziko lapansi.

Genesis 7