Genesis 50:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Farao anati, Pita kaike atate wako, monga iye anaku lumbiritsa iwe.

7. Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wace; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akuru a pa mbumba yace, ndi akuru onse a m'dziko la Aigupto,

8. ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ace, ndi mbumba ya atate wace: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.

9. Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magareta ndi apakavalo; ndipo panali khamc lalikuru.

10. Ndipo anafika pa dwale la Atadi, liri tsidya lija la Yordano, pamenepo anamlira maliro a atate wace masiku asanu ndi limodzi.

11. Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano.

12. Ndipo ana ace amuna anamcitira iye monga anawalamulira iwo;

Genesis 50