4. Atapita masiku akumlira iye Yosefe anati kwa mbumba ya Farao kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamase panu, nenanitu m'makutu a Parae kuti,
5. Atate wanga anandilumbi ritsa ine, kuti, Taona, ndirinkufa m'manda m'mene ndadzikonzeran ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundi loletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabwe ranso.
6. Ndipo Farao anati, Pita kaike atate wako, monga iye anaku lumbiritsa iwe.