30. Ndipo Yosefe anafulumira, cifukwa mtima wace unakhumbitsa mphwace, ndipo mafuna polirira; nalowa m'cipinda ace naliramo.
31. Ndipo anasamba ikhope yace, naturuka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani cakudya.
32. Ndipo anamuikira iye cace pa yekha, ndi wo cao pa okha, ndi Aaigupto ikudya naye cao pa okha; cifukwa aigupto sanathei kudya cakudya pamodzi ndi Ahebri: cifukwa kucita comweco nkunyansira Aaigupto.