23. Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu, ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu cum a m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawaturutsira Simeoni.
24. Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa aburu ao cakudya.
25. Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; cifukwa anamva kuti adzadya cakudya pamenepo.
26. Pamene Yosefe anadza kunyumba kwace, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.
27. Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? wokalamba uja amene nunanena uja: kodi alipo?
28. Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ili bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.