7. Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota.
8. Ndipo panali m'mamawa mtima wace unabvutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Aigupto, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lace; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
9. Pamenepo wopereka cikho wamkuru anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zocimwa zanga lero.
10. Farao anakwiya ndi anyamata ace, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkuru:
11. ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lace.