Genesis 40:21-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo anabwezanso wopereka cikho ku nchito yace; ndipo iye anapereka cikho m'manja a Farao.

22. Koma anampacika wophika mkate wamkuru; monga Yosefe anawamasulira.

23. Koma wopereka cikho wamkuru sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala.

Genesis 40