5. Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wace wamkazi; ana ace amuna anali ndi zoweta zace kudambo: ndipo Yakobo anakhala cete mpaka anafika iwo.
6. Ndipo Hamori atate wace wa Sekemu anaturuka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.
7. Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.
8. Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wace.
9. Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi.
10. Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kucita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.