Genesis 34:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

2. Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wace wamwamuna wa Hamori Mhivi, karonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa,

3. Ndipo mtima wace unakhumba Dina mwana wace wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

Genesis 34