Genesis 28:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, cifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wace, nagona tulo kumeneko.

12. Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pace ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.

13. Taonani, Yehova anaima pamwamba pace, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isake; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa Iwe ndi mbeu zako;

14. mbeu zako zidzakhala monga pfumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

15. Taonani, Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; cifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditacita cimene ndanena nawe.

16. Ndipo Yakobo anauka m'tulo tace, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

Genesis 28