26. Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.
27. Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
28. Mlungu akupatse iwe mame a kumwamba,Ndi zonenepa za dziko lapansi,Ndi tirigu wambiri ndi vinyo;
29. Anthu akutumikire iwe,Mitundu ikuweramire iwe;Ucite ufumu pa abale ako,Ana a amako akuweramire iwe;Wotemberereka ali yense akutemberera iwe,Wodalitsika ali yense akudalitsa iwe.
30. Ndipo panali atatha Isake kumdalitsa Yakobo, ataturuka Yakobo pamaso pa Isake atate wace, Esau mkuru wace analowa kucokera kuthengo,