Genesis 26:33-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo anacha dzina lace Seba, cifukwa cace dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.

34. Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Elone Mhiti:

35. ndipo iwo anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.

Genesis 26