Genesis 26:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Abimeleke anati kwa Isake, Ucoke kwa ife cifukwa kuti iwe uti wamkuru wopambana ife.

17. Ndipo Isake anacoka kumeneko, namanga hema wace m'cigwa ca Gerari, nakhala kumeneko.

18. Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wace; cifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazicha maina monga maina omwe anazicha atate wace.

19. Ndipo anyamata a Isake anakumba m'cigwa, napeza kumeneko citsime ca madzi otumphuka.

20. Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isake kuti, Madzi ndi athu; ndipo anacha dzina la citsimeco Eseke: cifukwa anakangana nave.

Genesis 26