Genesis 22:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lap ansi idzadalitsidwa: cifukwa wamvera mau anga.

19. Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ace, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.

20. Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;

21. Huzi woyamba ndi Buzi mphwace, ndi Kemueli atate wace wa Aramu;

22. ndi Kesede, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele.

23. Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwace wa Abrahamu.

24. Ndipo mkazi wace wamng'ono, dzina lace Rcuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.

Genesis 22