24. Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira.
25. Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleke cifukwa ca citsime ca madzi, anyamata ace a Abimeleke anacilanda.
26. Ndipo anati Abimeleke, Sindinadziwe amene anacita ico; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.
27. Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleke, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.
28. Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri pa okha.