32. tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu.
33. Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wace; ndipo sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka,
34. Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.
35. Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka.
36. Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.
37. Woyamba ndipo anabala mwana wamwamona, namcha dzina lace. Moabu; yemweyo ndi atate wa Amoabu kufikira lero.
38. Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namcha dzina lace Benammi; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.