3. Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwace; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda cotupitsa, ndipo anadya,
4. Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;
5. ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utiturutsire iwo kuti tiwadziwe.
6. Ndipo Loti anaturukira kwa iwo pakhomo, natseka cambuyo pakhomo pace.
7. Ndipo anati, Abale anga, musacitetu koipa kotere.