3. Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti,
4. Koma Ine, taona, pangano langa liri ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.
5. Sudzachedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; cifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.
6. Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzaturuka mwa iwe.
7. Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.