Genesis 13:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anakwera Abramu kucoka ku Aigupto, iye ndi mkazi wace, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera.

2. Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golidi,

3. Ndipo anankabe ulendowace kucokera ku dziko la kumwera kunka ku Beteli, kufikira kumalo kumene kunali hema wace poyamba paja, pakati pa Beteli ndi Ai;

Genesis 13