22. Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Ashuri, ndi Aripakasadi, ndi Ludi, ndi Aramu.
23. Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli, ndi Getere, ndi Masi.
24. Aripakasadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Ebere.
25. Kwa Ebere ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelege; cifukwa kuti m'masiku ace dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwace ndi Yokitani.
26. Ndipo Yokitani anabala Alamodadi, ndi Selefe, ndi Hazaramaveti, ndi Yera;