Genesis 1:22-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zicuruke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zicuruke pa dziko lapansi.

23. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu.

24. Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

Genesis 1