1. PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
2. Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi.
3. Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.
4. Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.
5. Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.