1. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
2. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israyeli, Kwatha; kwafika kutha kwace pa ngondya zinai za dziko.
3. Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zanse.