1. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndebvu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.
2. Limodzi la magawo ace atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapula-kwapula ndi lupanga pozungulira pace, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.
3. Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m'mkawo wa maraya ako.