3. Ndi m'malire a Aseri, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafitali, limodzi.
4. Ndi m'malire a Nafitali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.
5. Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efraimu, limodzi.
6. Ndi m'malire a Efraimu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.
7. Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.
8. Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale copereka a mucipereke, mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace, ndi m'litali mwace lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pace.
9. Copereka mucipereke kwa Yehova cikhale ca mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace.