Ezekieli 47:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndi malire ocokera kunyanja ndiwo Hazaremoni, ku malire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati, Ndiyo mbali ya kumpoto.

18. Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Gileadi, ndi dziko la Israyeli, ndiwo Yordano; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.

19. Ndi mbali ya kumwela kuloza kumwela ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meriboti Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, ndi ku nyanja yaikuru. Ndiyo mbali ya kumwela kuloza kumwela.

20. Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo nyanja yaikuru, kuyambira malire a kumwela kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo.

21. Motero mudzigawire dziko ili monga mwa mafuko a Israyeli.

22. Ndipo kudzacitika kuti muligawe ndi kucita maere, likhale colowa canu, ndi ca alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, alandire colowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israyeli.

23. Ndipo kudzatero kuti kupfuko kumene mlendo akhalako kumeneko mumpatse colowa cace, ati Ambuye Yehova.

Ezekieli 47