26. Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.
27. Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yace yaucimo, ati Ambuye Yehova.
28. Ndipo adzakhala naco colowa; Ine ndine colowa cao; musawapatsa colandira cao m'Israyeli; Ine ndine colandira cao.
29. Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; ndipo ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zao.