2. ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ace ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wace.
3. Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.
4. Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'kacisi kudzera njira ya cipata coloza kum'mawa.
5. Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane ku bwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu unadzaza kacisi.