Ezekieli 43:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israyeli kacisiyu, kuti acite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wace.

11. Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.

12. Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.

13. Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.

14. Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.

Ezekieli 43