Ezekieli 42:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.

2. Cakuno ca m'litali mwace mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwace mikono makumi asanu.

Ezekieli 42