Ezekieli 41:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pace pa nyumba; motero kupingasa kwace kwa nyumba kunakula kumwamba kwace, momwemonso anakwera kuyambira cipinda cakunsi, kupita capakati, kufikira cam'mwamba.

8. Ndinaonanso kuti kunyumba kunali ciunda pozungulira pace; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikuru.

9. Kucindikira kwa khoma la kuzipinda za m'mphepete kunja kwace kunali mikono isanu; ndipo mpata wace unali malo olowera m'zipinda za m'mphepete za kacisi.

10. Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pace ponse pa nyumba.

11. Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwela; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwace pozungulira pace.

12. Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwace; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pace linali la mikono isanu kucindikira kwace; ndi m'litali mwace mikono makumi asanu ndi anai.

13. Momwemo anayesa kacisi m'litali mwace mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ace, mikono zana limodzi;

Ezekieli 41