Ezekieli 41:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana cina pa cinzace; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa ku khoma locirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba.

7. Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pace pa nyumba; motero kupingasa kwace kwa nyumba kunakula kumwamba kwace, momwemonso anakwera kuyambira cipinda cakunsi, kupita capakati, kufikira cam'mwamba.

8. Ndinaonanso kuti kunyumba kunali ciunda pozungulira pace; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikuru.

9. Kucindikira kwa khoma la kuzipinda za m'mphepete kunja kwace kunali mikono isanu; ndipo mpata wace unali malo olowera m'zipinda za m'mphepete za kacisi.

10. Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pace ponse pa nyumba.

Ezekieli 41