1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, ndiye mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
3. nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
4. ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;