Ezekieli 37:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kucicita, ati Yehova.

15. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

16. Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israyeli anzace; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efraimu, ndi wa nyumba yonse ya Israyeli anzace;

17. nuiphatikize wina ndi unzace ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.

18. Ndipo ana a anthu amtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?

19. unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.

Ezekieli 37