4. Ndidzapasula midzi yako, nudzakhala lacipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5. Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israyeli ku mphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
6. cifukwa cace, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadana nao mwazi, mwazi udzakulondola.
7. Ndipo ndidzaika phiri la Seiri lodabwitsa ndi lacipululu, ndi kuononga pomwepo wopitapo ndi wobwerapo.