13. Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundicurukitsira mau anu ndawamva Ine.
14. Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lacipululu.
15. Monga momwe unakondwerera colowa ca nyumba ya Israyeli, papeza cidapasuka, momwemo ndidzakucitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.