21. Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,
22. cifukwa cace ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso cakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.
23. Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
24. Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.
25. Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zirombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'cipululu, ndi kugona kunkhalango.
26. Pakuti ndidzaika izi ndi miraga yozungulira citunda canga; zikhale mdalitso; ndipo ndidzabvumbitsa mibvumbi m'nyengo yace, padzakhala mibvumbi ya madalitso.
27. Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zace, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28. Ndipo sadzakhalanso cakudya ca amitundu, ndi cirombo ca kuthengo sicidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.