Ezekieli 32:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri, mwezi wakhumi ndi ciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aigupto nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nubvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.

3. Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakubvuulira m'khoka mwanga.

4. Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zirombe za dziko lonse lapansi ndi iwe.

5. Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako.

6. Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe.

7. Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nye nyezi zace; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace.

Ezekieli 32