Ezekieli 3:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.

11. Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.

12. Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukuru, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwace.

13. Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukuru.

14. M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kucoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa,

15. Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako woda bwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.

16. Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

17. Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, m'mwemo mvera mau oturuka m'kamwa mwanga, nundicenjezere iwo.

Ezekieli 3