10. Cifukwa cace taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira nsanja ya Sevene kufikira malire a Kusi.
11. Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.
12. Ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yace pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
13. Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aaigupto ku mitundu ya anthu kumene anamwazikirako;
14. ndipo ndidzabweza undende wa Aigupto, ndi kuwabwezera ku dziko la Patro, ku dziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka,