Ezekieli 27:34-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Muja unatyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.

35. Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri zikhululuka nkhope zao.

36. Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala coopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.

Ezekieli 27