7. cikufwa cace taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale cofunkha ca amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
8. Atero Ambuye Yehova, Popeza Moabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;
9. cifukwa cace taona, ndidzatsegula pambali pace pa Moabu kuyambira ku midzi, ku midzi yace yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Betiyesimoti, Baalameoni, ndi Kiriataimu,
10. kuwapereka kwa ana a kum'mawa pamodzi ndi ana a Amoni; ndipo ndidzawapereka akhale ao ao, kuti ana a Amoni asakumbukikenso mwa amitundu;
11. ndipo ndidzakwaniritsa maweruzo m'Moabu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
12. Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anacita mobwezera cilango pa nyumba ya Yuda, naparamula kwakukuru pakuibwezera cilango,